25 Mulungu angakulimbitseni pogwiritsa ntchito uthenga wabwino umene ndikulengeza ndiponso uthenga wonena za Yesu Khristu umene ukulalikidwa. Uthengawu ndi wogwirizana ndi zimene zaululidwa zokhudza chinsinsi chopatulika+ chimene chakhala chobisika kwa nthawi yaitali.