20 Ndinakhomereredwa pamtengo limodzi ndi Khristu.+ Si inenso amene ndikukhala ndi moyo,+ koma Khristu ndi amene ali ndi moyo ndipo ndi wogwirizana ndi ine. Zoonadi, moyo umene ndikukhala tsopano, ndikukhala mokhulupirira Mwana wa Mulungu,+ amene anandikonda nʼkudzipereka yekha chifukwa cha ine.+