28 nayenso Khristu anaperekedwa nsembe kamodzi kokha kuti anyamule machimo a anthu ambiri.+ Nthawi yachiwiri imene adzaonekere sadzaonekera nʼcholinga chochotsa uchimo. Ndipo amene adzamuone ndi anthu amene akumuyembekezera ndi mtima wonse kuti awapulumutse.+