1 Chivumbulutso chimene Yesu Khristu anapereka. Mulungu anamupatsa Chivumbulutso chimenechi+ kuti aonetse akapolo ake+ zinthu zimene zikuyenera kuchitika posachedwapa. Yesu anatumiza mngelo wake kuti adzapereke Chivumbulutsocho kwa kapolo wake Yohane+ pogwiritsa ntchito zizindikiro.