16 Mzindawo unali ndi mbali 4 zofanana kutalika kwake. Mulitali mwake nʼchimodzimodzi ndi mulifupi mwake. Mngeloyo anayeza mzindawo ndi bangolo ndipo anapeza kuti unali masitadiya 12,000 kuuzungulira. Mulitali mwake, mulifupi mwake ndiponso kuchoka pansi kupita mʼmwamba ndi zofanana.