14 Choncho Abulahamu anadzuka m’mawa kwambiri n’kutenga mkate ndi thumba la madzi lachikopa, n’kuziika paphewa pa Hagara.+ Atatero anamuuza kuti azipita limodzi ndi mwana wakeyo.+ Chotero Hagarayo ananyamuka n’kumangoyendayenda m’chipululu cha Beere-seba.+