17 Kwa Adamu, Mulungu ananena kuti: “Chifukwa wamvera mawu a mkazi wako, ndipo wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula+ kuti, ‘Usadzadye zipatso zake,’ nthaka ikhale yotembereredwa kwa iwe.+ Udzadya zotuluka m’nthakayo movutikira masiku onse a moyo wako.+