22 Mkazi aliyense adzapemphe zinthu zasiliva, zagolide, ndi zovala kwa munthu wokhala naye pafupi ndi kwa mlendo wamkazi wokhala m’nyumba mwake. Zinthu zimenezi mudzaveke ana anu aamuna ndi ana anu aakazi, ndipo mudzatenge zinthu zambiri za Aiguputo.”+