8 Ndiyeno Mose anapitiriza kuti: “Mudzaona zimenezi Yehova akakupatsani nyama yoti mudye madzulo ano, ndi mkate wokwanira m’mawa, chifukwa Yehova wamva kung’ung’udza kwanu kumene mukum’ng’ung’udzira. Ife ndife ndani? Kung’ung’udza kwanu si kotsutsana ndi ife, koma n’kotsutsana ndi Yehova.”+