19 “Kenako tinachoka ku Horebe ndi kuyenda kudutsa chipululu chachikulu ndi chochititsa mantha chonse chija+ chimene munachiona, podzera njira ya m’dera lamapiri la Aamori,+ monga momwe Yehova Mulungu wathu anatilamulira, mpaka tinafika ku Kadesi-barinea.+