-
Oweruza 16:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Koma Samisoni anagonabe mpaka pakati pa usiku. Kenako anadzuka pakati pa usikupo ndi kugwira zitseko za chipata cha mzinda+ pamodzi ndi nsanamira zake ziwiri, n’kuzizula pamodzi ndi mpiringidzo wake. Atatero anazinyamula pamapewa+ n’kupita nazo pamwamba pa phiri limene lili moyang’anana ndi Heburoni.+
-