-
1 Samueli 10:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Lero ukasiyana ndi ine, ukumana ndi amuna awiri pafupi ndi manda a Rakele+ pa Zeliza, m’dera la Benjamini. Iwo akuuza kuti, ‘Abulu aakazi+ amene unapita kukafunafuna anapezeka, moti bambo ako sakuganiziranso za abulu aakaziwo koma ayamba kudera nkhawa za inuyo, moti akunena kuti: “Nditani ine pakuti mwana wanga sakuoneka?”’+
-