14 Kenako m’bale wa bambo ake a Sauli anafunsa Sauli pamodzi ndi mtumiki wake kuti: “Kodi munapita kuti?” Poyankha iye anati: “Tinapita kukafunafuna abulu aakazi,+ moti tinali kungoyendabe kuwafufuza, koma sitinawapeze. Choncho tinapita kwa Samueli.”