24 Sauli nayenso anavula zovala zake, ndipo nayenso anayamba kuchita zinthu ngati mneneri pamaso pa Samueli. Iye anagwa pansi ndi kugona pomwepo ali wosavala usana wonse ndi usiku wonse.+ N’chifukwa chake pali mawu okuluwika akuti: “Kodi Sauli nayenso ndi mmodzi wa aneneri?”+