12 Kuwonjezera apo, pamene Abisalomu anali kupereka nsembe, anaitanitsa Ahitofeli+ Mgilo,+ phungu wa Davide,+ kuchoka kumzinda wakwawo wa Gilo.+ Chiwembu+ chimenecho chinapitiriza kukula ndipo chiwerengero cha anthu amene anali kutsatira Abisalomu chinapitiriza kuwonjezeka.+