13 Mfumu Solomo inapatsa mfumukazi ya ku Sheba zofuna zake zonse zimene inapempha, kuwonjezera pa zimene Mfumu Solomo inam’patsa malinga ndi kuwolowa manja+ kwa mfumuyo. Pambuyo pake, mfumukaziyo inatembenuka n’kubwerera kudziko lake, pamodzi ndi antchito ake.+