12 Atamva zimenezi mayiyo anati: “Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo,+ ndilibe mkate,+ koma ufa pang’ono+ mumtsuko waukulu ndi mafutanso pang’ono+ mumtsuko waung’ono. Panopa ndikutola tinkhuni kuti ndipite kukaphika chakudya choti ineyo ndi mwana wanga tidye. Tikadya, tiziyembekezera kufa.”+