12 Zimene zichitike n’zakuti ine ndikasiyana nanu, mzimu+ wa Yehova ubwera n’kukutengani kupita nanu kwina kumene ine sindikukudziwa. Ineyo ndikhala nditamuuza kale Ahabu, koma iyeyo sadzakupezani choncho adzandipha ndithu.+ Komatu mtumiki wanune ndakhala ndikuopa Yehova kuyambira ubwana wanga.+