23 M’chaka cha 7, Yehoyada+ analimba mtima n’kuitanitsa atsogoleri a magulu a asilikali 100,+ ndipo anachita nawo pangano. Atsogoleriwo anali Azariya mwana wa Yerohamu, Isimaeli mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maaseya mwana wa Adaya ndi Elisafati mwana wa Zikiri.