8 Alevi ndi Ayuda onse anachita mogwirizana ndi zonse zimene wansembe Yehoyada+ analamula.+ Choncho, aliyense anatenga amuna ake amene anali kulowa pa sabata, limodzi ndi amene anali kutuluka pa sabata,+ popeza wansembe Yehoyada anali asanawauze+ kuti azipita.