10 Iye anauza anthu onse kuti aimirire,+ kuyambira kumbali yakumanja ya nyumbayo mpaka kukafika kumbali yakumanzere ya nyumbayo. Anaimiriranso pafupi ndi guwa lansembe ndiponso pafupi ndi nyumbayo. Anthuwo anazungulira mfumuyo kumbali zonse, aliyense atatenga chida chake m’manja.