-
2 Mbiri 23:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Atatero anatenga atsogoleri a magulu a asilikali 100,+ anthu olemekezeka, atsogoleri a anthuwo, ndi anthu onse a m’dzikolo, n’kutsetsereka nayo mfumuyo kuchokera kunyumba ya Yehova.+ Anthuwo anadzera pachipata chakumtunda n’kukafika kunyumba ya mfumu. Kenako mfumuyo anaikhazika pampando wachifumu+ wa ufumuwo.
-