28 Mzimu wa Mulungu uli ngati mtsinje wosefukira umene wafika m’khosi,+ umene iye adzaugwiritsire ntchito posefa+ mitundu ya anthu monga zinthu zopanda pake. Pakamwa pa mitunduyo adzamangapo zingwe ngati zowongolera hatchi,+ zimene zidzawachititse kuyenda uku ndi uku.+