8 Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa madzi, umene mizu yake imakafika m’ngalande za madzi. Kutentha kukadzafika iye sadzadziwa, koma masamba ake adzachuluka ndi kukhala obiriwira.+ Pa nthawi ya chilala+ sadzada nkhawa kapena kusiya kubala zipatso.