11 “Anthu a ku Mowabu akhala mosatekeseka kuyambira pa unyamata wawo+ ndipo akukhalabe mosatekeseka ngati vinyo wansenga.+ Iwo sanatsanulidwepo kuchoka m’chiwiya china kupita m’chiwiya china ndipo sanapitepo ku ukapolo. N’chifukwa chake kukoma kwawo sikunawonjezeke ndipo fungo lawo silinasinthe.