26 Pamwamba pa thambo limene linali pamwamba pa mitu yawo, panali chinachake chooneka ngati mwala wa safiro,+ chooneka ngati mpando wachifumu.+ Pachinthu chooneka ngati mpando wachifumucho, panali winawake wooneka ngati munthu,+ atakhala pamwamba pake.