20 Chifukwa cha ine, nsomba zam’nyanja, zolengedwa zouluka zam’mlengalenga, zilombo zakutchire, zokwawa zonse zimene zimakwawa panthaka ndiponso anthu onse amene ali padziko lapansi, adzanjenjemera.+ Mapiri adzagwetsedwa,+ misewu yotsetsereka idzagumuka ndipo khoma lililonse lidzagwa pansi.’