18 “Malo otsala akhale aatali mofanana ndi malo omwe ndi chopereka chopatulika.+ Akhale mikono 10,000 kum’mawa ndiponso mikono 10,000 kumadzulo. Malo amenewo achite malire ndi malo omwe ndi chopereka chopatulika. Zokolola za pamalowo zizikhala chakudya cha otumikira mumzindawo.+