26 Kenako Nebukadinezara anayandikira khomo la ng’anjo yoyaka motoyo+ ndipo anati: “Sadirake, Mesake ndi Abedinego, inu atumiki a Mulungu Wam’mwambamwamba,+ tulukani ndipo mubwere kuno!” Zitatero, Sadirake, Mesake ndi Abedinego anatuluka pakati pa motopo.