-
Danieli 4:34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 “Pamapeto pa masiku amenewa,+ ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba+ ndipo nzeru zanga zinayamba kubwerera. Ndinatamanda Wam’mwambamwamba+ ndipo amene adzakhalapo mpaka kalekale ndinamutamanda ndi kumulemekeza,+ chifukwa ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo ufumu wake udzakhalapo ku mibadwomibadwo.+
-