8 Dzuwa litatuluka, Mulungu anatumiza mphepo yotentha yochokera kum’mawa.+ Dzuwalo linamutentha Yona pamutu moti anangotsala pang’ono kukomoka.+ Choncho Yona anapempha mobwerezabwereza kuti angofa. Iye anali kunena kuti: “Kuli bwino ndife kusiyana n’kuti ndikhale ndi moyo.”+