41 Tsopano anatenga mitanda ya mkate isanu ija ndi nsomba ziwiri zija n’kuyang’ana kumwamba ndi kupempha dalitso.+ Kenako ananyemanyema+ mitanda ya mkateyo ndi kuipereka kwa ophunzira ake kuti aipereke kwa anthuwo, ndiponso anaduladula nsomba ziwirizo ndi kugawira anthu onsewo.