21 Yesu anamuyang’ana ndipo anam’konda. Kenako anamuuza kuti: “Chinthu chimodzi chikusowekabe mwa iwe: Pita kagulitse zilizonse zimene uli nazo ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+