48 Koma amene sanadziwe+ ndipo wachita zinthu zofunika kum’kwapula zikoti, adzam’kwapula zikoti zochepa.+ Inde, aliyense amene anapatsidwa zambiri, zambirinso zidzafunika kwa iye.+ Ndipo aliyense amene anthu anamuika kuyang’anira zinthu zochuluka, anthuwo adzafunanso zochuluka kwa iye.+