22 “Amuna inu a mu Isiraeli, imvani mawu awa: Yesu Mnazareti,+ ndi munthu amene Mulungu anamuonetsera poyera kwa inu. Anatero mwa ntchito zamphamvu,+ mwa zodabwitsa komanso mwa zizindikiro, zimene Mulungu anachita pakati panu kudzera mwa iye,+ monga mmene inunso mukudziwira.