45 Ndipo makolo athu amene anachilandira kwa makolo awo, analowa nacho limodzi ndi Yoswa,+ m’dziko limene linali m’manja mwa anthu a mitundu ina+ amene Mulungu anawapitikitsa pamaso pa makolo athu.+ Chihemacho chinakhala m’dziko limeneli mpaka m’masiku a Davide.