11 Tsopano tamvera! Dzanja la Yehova lili pa iwe, ndipo ukhala wakhungu. Kwa kanthawi, suthanso kuona kuwala kwa dzuwa.” Nthawi yomweyo nkhungu yamphamvu ndi mdima wandiweyani zinamugwera, ndipo anafufuza uku ndi uku kufuna anthu oti amugwire dzanja ndi kumutsogolera.+