29 Pamenepo mumzindawo munadzaza chisokonezo, ndipo onse pamodzi anathamangira m’bwalo la masewera, atagwira Gayo ndi Arisitako n’kuwakokera m’bwalomo. Gayo ndi Arisitako+ anali anzake a Paulo amene anali kuyenda naye ndipo kwawo kunali ku Makedoniya.