9 panopa ndikukondwera. Sikuti ndikukondwera chifukwa munamva chisoni, koma chifukwa chakuti chisoni chimene munamvacho chinakuchititsani kulapa.+ Pakuti munamva chisoni mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu,+ chotero simunapwetekedwe m’njira iliyonse chifukwa cha zimene tinalemba.