Mawu a M'munsi
a Kodi nchiyani chimene munthu amene akudziŵa kuti ali ndi AIDS ayenera kuchita pamene akufuna kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova ndi kubatizidwa? Chifukwa cha kulemekeza malingaliro a ena, kungakhale kwabwino kwa iwo kupempha ubatizo wamtseri, ngakhale kuti palibe umboni wakuti AIDS yapatsiridwa kwa munthu kupyolera m’dziwe losambira. Pamene kuli kwakuti Akristu ambiri a m’zaka za zana loyamba anabatizidwa pa masonkhano aakulu apoyera, ena anabatizidwa mwamtseri chifukwa cha mikhalidwe yosiyanasiyana. (Mac. 2:38-41; 8:34-38; 9:17, 18) Njira ina ingakhale yakuti woyembekezera ubatizo wodwala AIDS abatizidwe pomaliza.