Mawu a M'munsi
a Mu 1844, mtsogoleri wachipembedzo Wachibritishi, E. B. Elliott, anasumika maganizo pa 1914 kukhala deti lothekera la mapeto a “nthaŵi zisanu ndi ziŵiri” za m’Danieli chaputala 4. Mu 1849, Robert Seeley, wa ku London, analongosola nkhaniyo mofananamo. Joseph Seiss, wa ku United States, anasonyeza 1914 kukhala deti lofunika kwambiri m’kuŵerengera zaka kwa Baibulo m’chofalitsidwa chokonzedwa pafupifupi mu 1870. Mu 1875, Nelson H. Barbour analemba m’magazini ake a Herald of the Morning kuti 1914 inali mapeto a nyengo imene Yesu anatcha “nthaŵi zawo za anthu akunja.”—Luka 21:24.