Mawu a M'munsi
b Amene afuna kumwa mankhwala ayenera kuonetsetsa kusiyana pakati pa kuipa ndi ubwino wake. Ayeneranso kuona ngati mantha awo ndi akulu mwakuti nkoyenera kumwa mankhwala. Akatswiri ambiri amaona kuti mankhwala angagwire ntchito bwino ngati mutaƔaphatikiza ndi chithandizo chokhudza mantha ndi khalidwe la munthuyo.