Mawu a M'munsi
a Mawu akuti BASE akuimira building, antenna, span, and earth (nyumba, zipilala zazitali, milatho, ndiponso zitunda zazitali). Maseŵera ameneŵa odumpha kuchoka pamwamba pa zinthu monga nyumba, milatho ndiponso zitunda zazitali akuti n’ngangozi kwambiri moti bungwe la National Park Service ku United States linawaletsa.