Mawu a M'munsi
a N’zoona kuti pankhani zina zovuta kwambiri, pangakhale zifukwa zoyenera kuti mwamuna kapena mkazi apatukane. (1 Akorinto 7:10, 11) Komanso, Baibulo limalola kusudzulana chifukwa cha chigololo. (Mateyu 19:9) Kuti munthu asudzule kapena asasudzule mnzake wosakhulupirika ndi nkhani ya aliyense payekha, ndipo ena sayenera kuumiriza wosalakwayo kuti aganize zosudzula mnzakeyo kapena ayi.—Onani buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, masamba 158-61, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.