Mawu a M'munsi
a Ngati m’dziko lanu anthu ambiri amagwiritsa ntchito chinsalu pozimira moto, onetsetsani kuti mumadziŵa kuchigwiritsa ntchito bwino. Bungwe la U.S. National Fire Protection Association linati: “Tikufuna kugogomeza kuti . . . nsalu zozimira moto n’zongogwirizira basi. Ziyenera kugwiritsidwa ntchito kokha ngati zilipo pafupi. . . . Kusagwiritsa ntchito bwino nsalu zozimira moto kungawonjezere utsi ndiponso kuvulala ndi moto ngati chinsalucho chitakhotetsera utsi kumaso kwa munthu kapena ngati chitapanda kuchotsedwa malaŵi akazima.”