Mawu a M'munsi
d Anthu amene amasuta fodya amadziika patsoka lalikulu kwambiri, chifukwa chakuti kusuta kumawononga mtima ndi njira zonse za magazi ndiponso kumachitsa kuti mitsempha ya magazi itsekeke pang’ono. Buku lina linati anthu 95 pa anthu 100 aliwonse amene amadulidwa chiwalo chinachake chifukwa cha matenda a shuga amakhala osuta fodya.