Mawu a M'munsi
e Ena mwa anthu ameneŵa ankalandira mankhwala akumwa. Ena mwa mankhwalaŵa amachititsa kuti kapamba azitulutsa mankhwala ambiri othandiza thupi kugwiritsira ntchito shuga, ena amachititsa kuti shuga asamachulukane kwambiri m’magazi, ndipo ena amachititsa kuti thupi lisalimbane ndi mankhwala ochokera m’kapamba. (Nthaŵi zambiri munthu akakhala ndi matenda a shuga a mtundu woyamba sam’patsa mankhwala akumwa.) Chifukwa chakuti pakali pano mankhwala a jakisoni wa matendaŵa amene alipo ngakuti munthu sangamwe chifukwa mphamvu yake imangothera m’mimba akamagayika motero siifika m’magazi. Sikuti munthu akamalandira jakisoni kapena mankhwala akumwawo ndiye kuti sayenera kuchita zinthu zolimbitsa thupi ndiponso kudya zamagulu.