Mawu a M'munsi
g Pafupifupi anthu 90 pa anthu 100 alionse odwala matenda a shuga amakhala ndi mtundu wachiŵiriwu. M’mbuyomu matenda a shuga a mtundu umenewu ankawatcha kuti ndi matenda osafunika mankhwala othandiza thupi kugwiritsira ntchito shuga kapenanso kuti ndi matenda ogwira munthu akakula. Komatu kunena choncho si kukhoza kwenikweni ayi, chifukwa chakuti anthu okwana mpaka 40 pa 100 aliwonse odwala matendaŵa amafunikira mankhwala othandiza thupi kugwiritsira ntchito shuga. Komanso, achinyamata ochuluka zedi, ena oti sanakwanitse n’komwe zaka 13, ayamba kumawapeza ndi mtundu umenewu wa matenda a shuga.