Mawu a M'munsi
a N’zoona kuti mtundu wa chakudya nawonso ndi wofunikira. Anthu a kumidzi mu Africa kaŵirikaŵiri amadya kwambiri zakudya za m’gulu la chimanga ndi ndiwo zamasamba kuposa anthu a m’tauni. Ndiponso nthaŵi zambiri amadya shuga wochepa, zakudya zochepa zokonzedwa ku fakitale, komanso amamwa zakumwa zoziziritsa kukhosi zochepa; zonsezitu zimawoletsa mano.