Mawu a M'munsi
b Ngati mayi akuona kuti akungokhala wosasangalala kwambiri ndiponso kuti palibenso chabwino chimene akuona m’moyo kapenanso ngati sakukonda mwana wake wakhanda ndi anthu enanso, ndiye kuti mwina ali ndi vuto losokonezeka maganizo limene ena amakhala nalo pambuyo pobereka. Ngati zili choncho, ayenera kufotokozera azamba. Onani Galamukani! ya August 8, 2002, masamba 14 mpaka 18 ndi Galamukani! ya Chingelezi ya June 8, 2003, masamba 21 mpaka 23.